Joshua 12
Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa
1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:2Sihoni mfumu ya Aamori,
amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,
amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.
8 ▼
24 ▼In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:9mfumu ya Yeriko | imodzi |
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli | imodzi |
10mfumu ya Yerusalemu | imodzi |
mfumu ya Hebroni | imodzi |
11mfumu ya Yarimuti | imodzi |
mfumu ya Lakisi | imodzi |
12mfumu ya Egiloni | imodzi |
mfumu ya Gezeri | imodzi |
13mfumu ya Debri | imodzi |
mfumu ya Gederi | imodzi |
14mfumu ya Horima | imodzi |
mfumu ya Aradi | imodzi |
15mfumu ya Libina | imodzi |
mfumu ya Adulamu | imodzi |
16mfumu ya Makeda | imodzi |
mfumu ya Beteli | imodzi |
17mfumu ya Tapuwa | imodzi |
mfumu ya Heferi | imodzi |
18mfumu ya Afeki | imodzi |
mfumu ya Lasaroni | imodzi |
19mfumu ya Madoni | imodzi |
mfumu ya Hazori | imodzi |
20mfumu ya Simuroni Meroni | imodzi |
mfumu ya Akisafu | imodzi |
21mfumu ya Taanaki | imodzi |
mfumu ya Megido | imodzi |
22mfumu ya Kadesi | imodzi |
mfumu ya Yokineamu ku Karimeli | imodzi |
23mfumu ya Dori ku Nafoti Dori | imodzi |
mfumu ya Goyini ku Giligala | imodzi |
24mfumu ya Tiriza | imodzi |
mafumu onse pamodzi analipo 31. |
Copyright information for
NyaCCL