Psalms 6
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.
1Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,kapena kundilanga mu ukali wanu.
2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;
Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.
Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;
Amakutamandani ndani ali ku manda?
6Ine ndatopa ndi kubuwula;
usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;
ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;
akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,
pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
9Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;
Yehova walandira pemphero langa.
10Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;
adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
Copyright information for
NyaCCL