‏ Psalms 73

BUKU LACHITATU

Masalimo 73–89

Salimo la Asafu.

1Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli,
kwa iwo amene ndi oyera mtima.

2Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka;
ndinatsala pangʼono kugwa.
3Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira,
pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.

4Iwo alibe zosautsa;
matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu.
5Saona mavuto monga anthu ena;
sazunzika ngati anthu ena onse.
6Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo;
amadziveka chiwawa.
7Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa;
zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.
8Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa;
mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.”
9Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba
ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi.
10Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo
ndi kumwa madzi mochuluka.
11Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji?
Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?”

12Umu ndi mmene oyipa alili;
nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira.

13Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera;
pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.
14Tsiku lonse ndapeza mavuto;
ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse.

15Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,”
ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
16Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi,
zinandisautsa kwambiri
17kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu;
pamenepo ndinamvetsa mathero awo.

18Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera;
Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke.
19Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa,
amasesedwa kwathunthu ndi mantha!
20Monga loto pamene wina adzuka,
kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye,
mudzawanyoza ngati maloto chabe.

21Pamene mtima wanga unasautsidwa
ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22ndinali wopusa ndi wosadziwa;
ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.

23Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;
mumandigwira dzanja langa lamanja.
24Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu
ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?
Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
ndi cholandira changa kwamuyaya.

27Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;
Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.
Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga
ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.
Copyright information for NyaCCL