‏ Psalms 74

Ndakatulo ya Asafu.

1Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu?
Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
2Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale,
fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola,
phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
3Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya
chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.

4Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe;
anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
5Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo
kuti adule mitengo mʼnkhalango.
6Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo
zonse zimene tinapachika.
7Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;
anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
8Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.”
Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
9Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa;
palibe aneneri amene atsala
ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.

10Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu?
Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
11Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja?
Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!

12Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale;
Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
13Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
14Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani
ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
15Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje,
munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
16Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso;
Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
17Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi;
munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.

18Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova,
momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
19Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo;
nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
20Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko
asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
21Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi;
osauka ndi osowa atamande dzina lanu.

22Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu;
kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
23Musalekerere phokoso la otsutsana nanu,
chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.
Copyright information for NyaCCL